2 Kings 17:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthuwo ankafukiza lubani ku akachisi onse, monga m'mene ankachitira anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraelewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nafukizapo zonunkhira pa misanje youse, monga umo amacitira amitundu amene Yehova adawacotsa pamaso pao, nacita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;