2 Kings 17:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo ao. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Adatsata milungu yachabechabe, ndipo iwo omwe adasanduka achabechabe. Ankatsata zitsanzo za anthu a mitundu ina okhala nawo pafupi, ngakhale Chauta anali atalamula kuti asamachite mofanana ndi mitundu imeneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakaniza malemba ace, ndi cipangano anacicita ndi makolo ao, ndi mboni zace anawacitira umboni nazo, natsata zopanda pace, nasanduka opanda pace, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asacite monga iwowa.