2 Kings 17:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta adakwiya nawo kwambiri Aisraele, ndipo adaŵachotsa osafuna kuŵaonanso. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalako, kupatula a fuko la Yuda okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova anakwiya naye Israyeli kwakukuru, nawacotsa pamaso pace osatsala mmodzi, koma pfuko la Yudalokha.