2 Kings 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adachita zoipa kuchimwira Chauta, komabe osalingana ndi mafumu a ku Israele amene ankalamulira, iyeyo asanaloŵe ufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi mafumu a Israeli amene ankalamulira iye asanalowe ufumuwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israyeli asanakhale iye.