2 Kings 17:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ataŵalekanitsa Aisraele kuŵachotsa pa banja la Davide, iwo adaika Yerobowamu mwana wa Nebati kuti akhale mfumu yao. Yerobowamuyo adaletsa Aisraele kuti asatsate Chauta, ndipo adaŵachimwitsa kwambiri Aisraelewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anang'amba Israele, kumchotsa kunyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati; Yerobowamu naingitsa Israele asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova atangʼamba Israeli kumuchotsa ku nyumba ya Davide, Aisraeliwo anasankha Yeroboamu mwana wa Nebati kukhala mfumu yawo. Yeroboamu ananyengerera Aisraeli kuti asatsatire Yehova ndipo anawachimwitsa tchimo lalikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anang'amba Israyeli, kumcotsa ku nyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati; Yerobiamu naingitsa Israyeli asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukuru.