2 Kings 17:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mpaka Chauta adaŵachotsa Aisraele kotheratu, monga momwe adaalankhulira kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Motero Aisraele adatengedwa ukapolo kuchoka ku dziko lakwao kupita ku Asiriya, ndipo ali kumeneko mpaka pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mpaka pamene Yehova anawachotsa pamaso pake monga anawachenjezera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Choncho Aisraeli anachotsedwa mʼdziko lawo kupita ku ukapolo ku Asiriya ndipo ali komweko mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mpaka Yehova adacotsa Israyeli pamaso pace, monga adanena mwa dzanja la atumiki ace onse aneneriwo. Momwemo Israyeli anacotsedwa m'dziko lao kumka nao ku Asuri mpaka lero lino.