2 Kings 17:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriya idabwera ndi anthu kuchokera ku mizinda ya Babiloni, Ava, Hamati ndi Sefaravaimu, nkudzaŵakhazika ku dziko la Samariya m'malo mwa Aisraele amene adatengedwa ukapolo. Tsono anthuwo adaloŵa m'midzi ya Samariyayo naisandutsa yaoyao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m'midzi mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Asiriya inabweretsa anthu a ku Babuloni, Kuta, Awa, Hamati ndi a ku Sefaravaimu kudzawakhazika mʼmizinda ya Samariya kulowa mʼmalo mwa Aisraeli. Iwo anatenga Samariya ndi kukhala mʼmizinda yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Asuri anabwera nao anthu ocokera ku Babulo, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Safaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israyeli; nakhala iwo eni ace a Samariya, nakhala m'midzi mwace.