2 Kings 17:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mfumu ya ku Asiriya idamva kuti, “Anthu a mitundu ina aja amene mudaŵakhazika m'midzi ya ku Samariya, sakudziŵa kupembedza Mulungu wa dzikolo. Nchifukwa chake Mulungu adaŵatumizira mikango pakati pao, ndipo ikuŵapha, chifukwa sakuchita zimene Mulunguyo akufuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero ananena ndi mfumu ya Asiriya, kuti, Amitundu aja mudawachotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; chifukwa chake anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, ilikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumu ya ku Asiriya inawuzidwa za nkhaniyi kuti, “Anthu amene munawatumiza ndi kuwakhazika mʼmizinda ya Samariya sakudziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna. Choncho Iye watumiza mikango pakati pawo imene ikuwapha chifukwa anthuwo sadziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero ananena ndi mfumu ya Asuri, kuti, Amitundu aja mudawacotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; cifukwa cace anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, irikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.