2 Kings 17:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mtundu uliwonse wa anthuwo unkapangabe mafano a milungu yaoyao, ndipo ankaika milunguyo m'nyumba zachipembedzo zimene Asamariya adaazimanga. Mtundu uliwonse wa anthuwo unali ndi nyumba za mulungu wao ku mzinda uliwonse kumene ankakhala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma a mtundu uliwonse anapanga milungu yaoyao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uliwonse m'midzi mwao mokhala iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mtundu uliwonse wa anthu unkapangabe mafano a milungu yawoyawo mʼmizinda yambiri imene anthuwo ankakhala, ndipo anayika milunguyo mʼnyumba za milungu zimene anthu a ku Samariya anamanga ku malo opembedzera mafano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma a mtundu uli wonse anapanga milungu yao yao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uli wonse m'midzi mwao mokhala iwo.