2 Kings 17:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo ankapembedzanso Chauta nadzisankhira pakati pao anthu wamba, kuti akhale ansembe otumikira ku nyumba zao zachipembedzo. Ansembe amenewo ndi amene ankaperekera anthu nsembe m'nyumba zopembedzeramo milungu yao ku zitunda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ankapembedza Yehova, koma ankadzisankhira okha pakati pawo anthu wamba kuti akhale ansembe awo ku nyumba za milungu za ku malo opembedzera mafano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje.