2 Kings 17:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuchitabe zimene ankachita kale mpaka lero lino. Iwowo salemekeza Chauta kwenikweni ndipo satsata zogamula kapena zolengeza, ngakhale malangizo kapena malamulo amene Chauta adalamula zidzukulu za Yakobe, amene adamtchula kuti Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mpaka lero lino acita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sacita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena cilamulo, kapena coikika adacilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamucha Israyeli,