2 Kings 17:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma muzipembedza Ine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito ndi mphamvu zanga zazikulu ndi mkono wanga wokutetezani. Muzigwadira Ine Chauta, ndipo muzipereka nsembe kwa Ine ndekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndiye amene muyenera kumupembedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma Yehova amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;