2 Kings 17:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsiku lina mfumu ya ku Asiriya idaona kuti Hoseya akuchita zaupandu. Ndiye kuti Hoseyayo anali atatuma amithenga kukapempha chithandizo kwa So, mfumu ya ku Ejipito, Ndiponso adaaleka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, m'menemo kale ankakhoma chaka ndi chaka. Nchifukwa chake mfumu ya ku Asiriya itamva zimenezi, idamanga Hoseya ndi kumuika m'ndende.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mfumu ya ku Asiriya inazindikira kuti Hoseya akuwukira, pakuti Hoseyayo anali atatumiza nthumwi kwa So mfumu ya Igupto ndiponso analeka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, monga ankachitira chaka ndi chaka. Choncho Salimenezeri anagwira Hoseya ndi kumuyika mʼndende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu ya Asuri anampeza Hoseya alikucita ciwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Aigupto, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asuri, monga akacita caka ndi caka; cifukwa cace mfumu ya Asuri anamtsekera, nammanga m'kaidi.