2 Kings 17:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mitundu ya anthu imeneyi inkapembedza Chauta, kwinaku nkumatumikira milungu yao yachabechabe ija. Ana ao adachitanso zomwezo, adzukulu ao adachita zokhazokhazo zimene ankachita makolo ao, ndipo akuchitabe zomwezo mpaka pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale anthuwo ankapembedza Yehova, ankatumikiranso mafano awo. Mpaka lero lino ana awo ndi zidzukulu zawo zikupitiriza kuchita zomwe ankachita makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anacita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.