2 Kings 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Asiriya idagonjetsa Samariya, ndipo idatenga Aisraele kuŵachotsa kwao kupita nawo ku Asiriya. Idaŵakhazika ena ku mzinda wa Hala, ena kufupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndipo enanso ku mizinda ya Amedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya, mfumu ya ku Asiriya inalanda Samariya ndipo inatenga Aisraeli ndi kupita nawo ku Asiriya. Anakawakhazika ku Hala ndi Habori mʼmbali mwa mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Asuri analanda Samariya, natenga Aisrayeli andende, kumka nao ku Asuri; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.