2 Kings 17:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezo zidaoneka chifukwa Aisraele adachimwira Chauta Mulungu wao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, kuŵachotsa m'manja mwa Farao mfumu ya ku Ejipito. Aisraelewo ankapembedza milungu ina,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kudatero, popeza ana a Israyeli adacimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwaturutsa m'dziko la Aigupto pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, ndipo anaopa milungu yina,