2 Kings 17:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aisraele ankachita zinthu zoipa mobisika namachimwira Chauta Mulungu wao. Adadzimangira akachisi opembedzerako mafano ku midzi yao yonse ndi ku mizinda yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anachita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumudzi walinga komwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anacita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse ku nsanja ya olonda ndi ku mudzi walinga komwe.