2 Kings 18:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaulanda patapita zaka zitatu. Chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Hezekiya chimene chinali cha chisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Israele, mzinda wa Samariya udalandidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakutha pake pa zaka zitatu anaulanda, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Israele analanda Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asiriya analanda mzindawu patatha zaka zitatu. Choncho mzinda wa Samariya unalandidwa chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya mfumu ya Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakutha pace pa zaka zitatu anaulanda, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Israyeli analanda Samariya.