2 Kings 18:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Asiriya idatenga Aisraele kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya. Adakaŵakhazika ku mzinda wa Hala, ndinso pafupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndi ku mizinda ya Amedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Asiriya anachotsa Aisraele kunka nao ku Asiriya, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Asiriya inatenga Aisraeli kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya ndipo anakawakhazika ku Hala, ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Asuri anacotsa Aisrayeli kumka nao ku Asuri, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi;