2 Kings 18:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Izi zidachitika chifukwa choti anthuwo sadamvere mau a Chauta Mulungu wao, koma adaphwanya chipangano chake, pamodzi ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Chauta adaŵalamula. Sadatsate zimenezo kapena kuzigwiritsa ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira chipangano chake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zinachitika chifukwa sanamvere zonena za Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula. Iwo sanamvere malamulowo kapena kuwagwiritsa ntchito.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa sanamvera mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira cipangano cace, ndico zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvera kapena kuzicita.