2 Kings 18:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Hezekiya mfumu ya ku Yuda adatumiza mau ku Lakisi kwa mfumu ya ku Asiriya, onena kuti, “Ndidalakwa ine. Lekeni. Chilichonse chimene munene ndidzachita.” Pamenepo mfumu ya ku Asiriya idamlamula Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, kuti azipereka makilogramu a siliva okwanira 3,000 ndi makilogramu a golide 1,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asiriya ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundichokere; chimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asiriya anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya ku Asiriya ku Lakisi wonena kuti, “Ine ndalakwa. Chokani kuno ndipo ndidzakupatsani chilichonse chimene munene.” Mfumu ya ku Asiriya inalamula mfumu Hezekiya, mfumu ya Yuda, kuti azipereka makilogalamu a siliva okwana 3,000 ndi makilogalamu a golide 1,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundicokere; cimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.