2 Kings 18:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe mfumu ya ku Asiriya idatuma mtsogoleri wankhondo, nduna yaikulu ndi kazembe wankhondo, pamodzi ndi gulu lankhondo lalikulu kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwowo adapita nakafika ku Yerusalemu, ndipo adakaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri wa nsalu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsalu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Asiriya inatuma Taritani, Rabusarisi ndi Rabusake pamodzi ndi gulu lalikulu la ankhondo, kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwo anafika ku Yerusalemu nakayima pafupi ndi ngalande ya madzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu waukulu wopita ku malo a Munda wa Mmisiri Wochapa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Asuri anatuma nduna ndi ndoda ndi kazembe ocokera ku Lakisi ndi khamu lalikuru la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima ku mcerenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsaru.