2 Kings 18:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza ati. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kumbaya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzamlowa m'dzanja lake ndi kuliboola; atero Farao mfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Aigupto; ndilo munthu akatsamirapo lidzamlowa m'dzanja lace ndi kulibola; atero Farao mfumu ya Aigupto kwa onse omkhulupirira iye.