2 Kings 18:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu. Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pano m'Yerusalemu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, “Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa lansembe ili mu Yerusalemu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamcotsera misanje yace ndi maguwa a nsembe ace, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pane m'Yerusalemu?