2 Kings 18:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ungathe bwanji kupambana ngakhale mmodzi yekha mwa akazembe ang'onoang'ono a mbuye wanga, pamene ukukhulupirira Aejipito, kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Ejipito akupatse magaleta ndi apakavalo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Aigupto akupatse magareta ndi apakavalo?