2 Kings 18:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, ndiponso Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe m'Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina ndi Yowa anawuza Rabusakeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.