2 Kings 18:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomawo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? Si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Rabusake anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?