2 Kings 18:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzachita choncho mpaka nthaŵi imene mfumuyo idzakutengeni kupita nanu ku dziko lolingana ndi lanuli, dziko la chonde la mwana alirenji, kuti kumeneko mudzakhale moyo, osafa. Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mpaka nditabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanuli, dziko la tirigu ndi vinyo watsopano, dziko la chakudya ndi minda ya mipesa, dziko la mitengo ya olivi ndi uchi. Sankhani moyo osati imfa! “Musamvere zonena Hezekiya, pakuti iye akukusocheretsani ponena kuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uci; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.