2 Kings 18:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Eliyakimu mwana wa Hilikiya, amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu, mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza Hezekiya zonse zimene anayankhula Rabusake uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.