2 Kings 18:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaononga akachisi onse opembedzerako mafano, nagwetsa zipilala zamiyala, nkuthyolanso mitengo ya Asera. Kenaka adatswanya njoka yamkuŵa ija imene adapanga Mose, popeza kuti mpaka masiku amenewo, Aisraele ankaifukizira lubani pofuna kuilemekeza njokayo. Ankaitchula kuti Nehusitani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachotsa malo opembedzerako mafano, anaphwanya miyala yachipembedzo ndiponso anadula mafano a Asera. Iye anaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, pakuti mpaka kufikira nthawi imeneyi Aisraeli amafukiza lubani kwa njoka imeneyi. (Imatchedwa Nehusitani).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.