2 Kings 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chachinai cha ufumu wa Hezekiya chimene chinali chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Hoseya, mwana wa Ela, mfumu ya ku Israele, Salimanezere mfumu ya ku Asiriya adabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya, ndipo adauzinga ndi zithando zankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Salimenezeri, mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya ndi kuwuzinga
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali caka cacinai ca mfumu Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli Salimanezeri mfumu ya Asuri anakwerera Samariya, naumangira misasa.