2 Kings 19:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udatuma amithenga ako kudzandinyoza Ine, ndipo udati, ‘Ndi magareta anga ochuluka ndidakwera mapiri ataliatali, ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni. Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri, ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa. Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni, m'nkhalango yake yoŵirira kwabasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudzera mwa amithenga ako wonyoza Ambuye. Ndipo wanena kuti, ‘Ndi magaleta ochuluka ndinakwera mapiri ataliatali, pa msonga za mapiri a Lebanoni. Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri, mitengo yake ya payini yabwino kwambiri. Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni, mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magareta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zace za Lebano, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yace yaitali, ndi mitengo yace yosankhika yar mlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwace mweni mweni, ku nkhalango zace za madimba.