2 Kings 19:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma Ine Chauta ndikuti, Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale? Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana, tsopano ndazichitadi. Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga ndi kuisandutsa miyulu ya miyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula midzi yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Kodi sunamvepo? Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale. Ndinazikonzeratu masiku amakedzana; tsopano ndachita kuti zichitikedi, iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa kukhala milu ya miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sunamva kodi kuti Ine ndinacicita kale lomwe, ndi kucipanga masiku akalekale? tsopano ndacifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula imidzi yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.