2 Kings 19:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene ankakhala kumeneko anali opanda mphamvu, ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka. Anali ngati mbeu zam'munda, ngati udzu wanthete. Anali ngati udzu wapadenga, umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake okhalamo ao anali ofooka manja, anaopsedwa, nachita manyazi, ananga udzu wa kuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu, athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi. Ali ngati mbewu za mʼmunda, ngati udzu wanthete, ali ngati udzu womera pa denga, umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace okhalamo ao anali ofok a manja, anaopsedwa, nacita manyazi, ananga udzu wa kuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.