2 Kings 19:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chakuti udandikwiyira, ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza, ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako. Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira yomwe udadzera pobwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera pa njira unadzerayi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chakuti wandikwiyira ndipo ndamva za mwano wako, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako, ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa njira yomwe unadzera pobwera.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cam'kamwa canga m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera pa njira unadzerayi.