2 Kings 19:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti, “Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi: Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa. Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera. Tsono chaka chamkucha mudzafesa tirigu nkukolola, mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi: “Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa, ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera. Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola, mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ici ndi cizindikilo cako: caka cino mudzadya za mphulumukwa, ndi caka ca mawa za mankhokwe, ndi caka camkuca muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zace.