2 Kings 19:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya ndi izi, akuti, ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu, sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe. Ankhondo ake azishango sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu, ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzalowa m'mudzi muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi: “ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu kapena kuponyamo muvi. Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, iye sadzalowa m'mudzi muno, kapena kuponyamo mubvi, kapena kufikako ndi cikopa, kapena kuundira mtumbira.