2 Kings 19:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipokunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wace, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarihadoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.