2 Kings 19:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Asiriya yatuma kazembe wake wankhondo kudzanyoza Mulungu wamoyo. Makamaka Chauta, Mulungu wanu, wamva kunyoza kumeneku, ndipo adzaŵalanga anthu amene adamunyozawo. Nchifukwa chake muŵapempherere anthu otsalaŵa amene akali ndi moyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asuri mbuye wace, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga cifukwa ca mau adawamva Yehova Mulungu wanu; cifukwa cace uwakwezere otsalawo pemphero.