2 Kings 19:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kumka ku dziko lace, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lace.