2 Kings 19:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asuri alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adacoka ku Lakisi.