2 Kings 19:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mau onena kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, waturuka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,