2 Kings 2:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Eliya adauza Elisayo kuti, ‘Wapempha chinthu chapatali. Komabe ukandipenya pa nthaŵi imene ndikukusiya, zimene wapemphazi zidzakuchitikiradi. Koma ukapanda kundipenya, sizidzachitika.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Wapempha chinthu chapatali, koma ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Wapempha cinthu capatali, koma ukandipenya pamene ndicotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero at.