2 Kings 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwowo akuyendabe ndi kumakamba, adangoona galeta lamoto ndi akavalo ake amoto zikuŵasiyanitsa aŵiriwo. Ndipo Eliya adakwera kumwamba m'kamvulumvulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacidka, akali ciyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka gareta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kabvumvulu.