2 Kings 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisa adaona zimenezi nafuula kuti, “Bambo wanga, Bambo wanga! Magaleta a Aisraele ndi anthu ake okwera pa akavalo.” Ndipo sadamuwonenso Eliyayo. Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing'amba paŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa anapenya, napfuula, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zobvala zace zace, nazing'amba pakati.