2 Kings 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adagwira mwinjiro wa Eliyawo namenya nawo madzi aja, nati, “Ali kuti Chauta, Mulungu wa Eliya?” Atamenya madziwo choncho, madzi aja adapatukana, ena kwina, ena kwina. Ndipo Elisa adaoloka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Elisa anatenga chovala chomwe chinagwa kuchokera kwa Eliya napanda nacho madzi. Iye anafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wa Eliya?” Atapanda madzi, madziwo anagawika pakati, ena kwina ena kwina, ndipo iye anawoloka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatenga copfunda ca Eliya cidamtayikiraco, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.