2 Kings 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo iwo adamuuza kuti, “Taonani tsono, ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Chonde mulole kuti anyamuke akamufunefune mbuyanu Eliya. Mwina mwake mzimu wa Chauta wamtenga nkukamponya kuphiri kwina kapena ku chigwa.” Elisayo adati, “Iyai musaŵatume.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.” Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tiri nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'cigwa dna. Koma anati, Musatumiza.