2 Kings 2:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma adamkakamiza mpaka Elisayo mwamanyazi adaŵalola naŵauza kuti, “Chabwino, atumeni.” Ndiye iwo adaŵatuma anthu makumi asanuwo. Ndipo anthuwo adakafunafuna Eliya masiku atatu, koma osampeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anamuumiriza kufikira anachita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anamukakamizabe mpaka Elisayo anachita manyazi moti sakanatha kukana. Choncho iye anati, “Atumizeni.” Ndipo anatumiza anthu makumi asanu amene anakafunafuna Eliya kwa masiku atatu koma sanamupeze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anamuumiriza kufikira anacita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.