2 Kings 2:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Elisa adapita ku kasupe wa madzi, nathiramo mchere m'kasupemo, nati, “Chauta akunena kuti, ‘Madzi ameneŵa ndaŵakonza. Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo, m'madzi ameneŵa simudzakhala chinthu chopha anthu kapena choletsa nthaka kubereka.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka kumka ku magwero a madzi, nathiramo mcere, nati, Atero Yehova, Ndaciritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.