2 Kings 2:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono a m'gulu la aneneri amene anali ku Beteleko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a aneneri a ku Beteli anabwera kwa Elisa namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?” Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma musakambe zimenezi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a aneneri okhala ku Beteli anaturukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, lode ndidziwa, khalani muli cete.